Bungwe la boma logula, kusunga ndi kugulitsa chimanga la ADMARC tsopano lili ndi bodi yatsopano yoyendetsa bungweli.
Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe watulutsa Peter Sambani, mkulu oyendetsa kampani za boma mdziko muno.
Malingana ndi Chikalatacho, Counsel Pempho Likongwe ndi yemwe wasankhidwa ngati wa pampando wa bodi imeneyi.
Ndipo wena omwe asankhidwa ngati ma membala a bodi imeneyi ndi monga Inkosi Msakambewa, Selia Msiska, Olivia Chaju Liwewe, Daniel Alfred Chatonya, komanso Alfred Tcherani.
Bodi yatsopanoyi inayamba kugwira ntchito zake kuyambira mwezi watha pa 26 mwezi watha wa March.
Pakali pano, Sambani mchikalatacho, wati boma lili ndi chikhulupiliro kuti bodi yatsopanoyi ithandiza kwambiri kupititsa patsogolo ntchito za ADMARC mdziko muno.