Timu ya Silver Strikers yalora kusewera masewero ake pa bwalo la Bingu

Kusamvana komwe kunalipo pakati pa bungwe loyendetsa masewero a mpira a mu mpikisano wa Super League, la SULOM ndi timu ya Silver Strikers tsopano kwatha.


Kusamvanaku kunabuka potsatira ganizo la bungwe la SULOM loyika masewero a loweruka likudzali, a pakati pa timu ya Silver Strikers ndi Nyasa Big Bullets pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.


Izi sizinakondweretse timu ya Silver Strikers yomwe mu chikalata chomwe inatulutsa posachedwapa inatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sipita pa bwalo la za masewero la Bingu kukasewera masewerowo.


Malinga ndi Patrick Chimimba yemwe ndi mkulu oyendetsa ntchito za Silver Strikers, iwo samafuna kukasewera masewerowo pa bwaloli poganizira kuti iwo ali ndi bwalo lawo la Silver Stadium lomwe amayenera kumasewelera masewero awo a pa khomo.


Chimimba anatinso bungweli linalakwitsa kuyika masewerowo pa bwalo la Bingu popanda kufunsa maganizo a timuyi.


Koma bungwe la SULOM lakhala likutsindika kuti linaganiza zoyika masewerowo pa bwalo la Bingu podziwa kukula kwa masewerowa, omwe mwa zina ndi ofunika chitetezo chokhwima, chomwe sichingatheke pa Silver Stadium.


Chomcho potsatira zokambirana zomwe zakhala zikuchitika pakati pa mbali ziwirizi, timu ya Silver Strikers tsopano yavomera zokasewera masewerowa pa bwalo la Bingu, zomwe zakondweretsa bungwe la SULOM.


Malingana ndi Gilbert Mitawa yemwe ndi mtsogoleri wa bungwe la SULOM, kunyanyala masewerowa chifukwa choti achitikira pa bwalo la Bingu sikunakapereka chithunzi chabwino cha timu ya Silver Strikers.


Chomcho Mitawa wathokoza timuyi chifukwa chovomera kukasewera pa bwalo la Bingu.

Related posts

SULOM yapereka zifukwa zokwezera mtengo wa masewero

Boma lati lilemba ogwira ntchito za umoyo mdziko muno

Apolisi ati asintha kagwiridwe ka ntchito