Timu ya mpira wa miyendo yomwe osewera ake ndi atsikana yalimbikitsa zokonzekera zake za masewero awiri a pa ubale ndi timu ya dziko la South Africa.
Masewero ongopimana mphamvuwa aseweredwa loweruka likudzali pa 5 April komanso la chiwiri sabata ya mawa pa 8 April, 2025.
Koma mu masewerowa, timu ya dziko lino idzakhala opanda atatu mwa osewera ake odalilika kwambiri, omwe ndi Temwa Chawinga, Tabitha Chawinga komanso Rose Kabzere.
Malingana ndi bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la Football Association of Malawi (FAM), osewera atatuwa sakhala nawo pa masewerowo chifukwa cha kuchedwa kwa dziko la South Africa kutsimikiza za masewerowo, zomwe zapangitsa kuti kukhale kovuta kuti atatuwa akwanitse kufika mdziko kudzachita nao zokonzekera za masewerowo mu nthawi yake.
Komabe osewera wena a timu ya Scorchers omwe amasewera mu ma kalabu a kunja kwa dziko lino, monga Vanessa Chikupira, Sabina Thom, komanso Chimwemwe Madise akuyembekezeka kudzakhala nawo pa masewerowo.
Masewerowa akuyembekezeka kuthandiza kwambiri timu ya dziko lino kukonzekera bwino masewero ake ndi timu ya Angola opeza malo mu chikho cha masewero a mpira wa miyendo wa amayi, omwe adzachitike mu mwezi wa October chaka chino.
Masewero a mu ndime yomaliza ya chikhochi adzachitika chaka cha mawa kuyambira pa 5 mpaka pa 26 July mdziko la Morocco.