SULOM yapereka zifukwa zokwezera mtengo wa masewero

Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo a mu mpikisano wa Super League la SULOM lafotokoza chifukwa chomwe chachititsa kuti likweze mulingo wa ndalama zomwe anthu amalipira pokaonera masewero a mu mpikisanowu.


Malingana ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa, bungweli latsindika kuti lachita chiganizo chokweza mtengowu kamba ka kukwera mtengo kwa zinthu zosiyana siyana zomwe bungweli limagwiritsa ntchito pokonzekera masewero a mpira.


Kamba ka ichi, mulingo wa ndalama zomwe anthu adzilipira akafuna kuonera masewero a mpira a mu mpikisanowu akwera ndi ndalama yokwana K1000 pa mulingo ulionse.


Masewerowa ndi monga okhudza ma timu akulu akulu a mdziko muno omwe afika pa mtengo wa K5000 kuchoka pa K4000 chaka chatha.


Masewero ena omwe mtengo wake wakwezedwanso ndi a matimu akulu pang’ono omwe achoka pa mtengo wa K3000, monga momwe analili chaka chatha, ndipo chaka chino anthu owonera adzilipira ndalama zokwana K4000.


Ndipo kuonjezera apo, bungwe la SULOM lakwezanso mtengo owonera masewero a matimu ang’ono ang’ono kuchoka pa K2000, monga zinalili chaka chatha, kufika pa mtengo wa K3000.

Related posts

Boma lati lilemba ogwira ntchito za umoyo mdziko muno

Apolisi ati asintha kagwiridwe ka ntchito

Olemba nkhani aziteteze pa nthawi yazipolowe