Olemba nkhani aziteteze pa nthawi yazipolowe

Atola nkhani mdziko muno awapempha kuti ateteze moyo wao pa nthawi yomwe akutola ndi kulemba nkhani zokhudza zipolowe.


Langizoli laperekedwa pa maphunziro a tsiku limodzi omwe bungwe la Media Council of Malawi (MCM) linakonza mu mzinda wa Blantyre.


Maphunzirowa anakonzedwa ngati njira imodzi yokonzetsera olemba nkhani momwe angagwilire ntchito zao mu nyengo za zipolowe zakudza kamba ka zionetsero kapena zisankho.


Popereka pempholi, Moses Kaufa yemwe ndi mkulu wa bungwe la MCM wati ndi kofunika kuti olemba nkhani adzilumikizana bwino ndi a polisi pomwe akuona kuti moyo wao uli pa chiopsezo pa nthawi yomwe akugwira ntchito yao mu nthawi ngati zimenezi.


Mmau ake, Harry Namwaza yemwe ndi mneneri wa apolisi mdziko muno wati a polisi ndi okonzeka kupereka chitetezo kwa olemba nkhani pomwe akumana ndi chiopsezo pa moyo wao pomwe akugwira ntchito yao.


Ndipo izi kuti zichitike, Namwaza anapempha olemba nkhaniwa kuti adzidziwitsa mwachangu a polisi pomwe akumana ndi mavuto a mtundu otere.

Related posts

SULOM yapereka zifukwa zokwezera mtengo wa masewero

Boma lati lilemba ogwira ntchito za umoyo mdziko muno

Apolisi ati asintha kagwiridwe ka ntchito