ODWALA PA CHIPATALA CHA NGABU SAKULANDIRA CHAKUDYA KWA CHAKA TSOPANO.

 

 

Patha pafupifupi chaka odwala omwe agonekedwa pa chipatala cha Ngabu asakulandira chakudya chilichonse chophikidwa pa chipatalachi, popanda chifukwa chodziwika bwino.

Malingana ndi kafukufuku yemwe wailesi ya Chibvomerezi yakhala ikuchita, chipatalachi chinasiya kuphika kapena kupereka zakudya kwa odwala kuyambira m’mwezi wa May chaka chatha.

Chomwe chinayimitsa chikonzerochi sichikudziwika mpaka pano, ndipo ntchito yofufuza za vutoli ili mkati pa chipatalapa.

Ophika a pa chipatalachi akhala akutitsina khutu kuti akhala asakulandira katundu ndi zakudya zoti adziwakonzera odwalawa kuchokera ku chipatala chachikulu cha m’boma la Chikwawa.

Ndipo sabata zingapo zapitazo, atafunsidwa pa nkhaniyi koyamba ndi wailesi ya Chibvomerezi, mneneri ku ofesi ya za umoyo ya mboma la Chikwawa, a Settie Piriminta, anapempha kuti apatsidwe nthawi yokwanira kuti afufuze vutoli.

Koma a Piriminta atsimikiza kuti odwala pa chipatala cha Ngabu akhala asakulandiradi chakudya.

Choncho iwo ati posachedwapa akhala akufotokozera wailesi ino chomwe chikuchititsa vutoli akafufuzabe za nkhaniyi.

#malawi #Chibvomelezifmnews

Related posts

SULOM yapereka zifukwa zokwezera mtengo wa masewero

Boma lati lilemba ogwira ntchito za umoyo mdziko muno

Apolisi ati asintha kagwiridwe ka ntchito