Ophunzira a msukulu za ukachenjede omwe sangathe kudzilipilira okha ndalama za maphunziro awo tsopano ali ndi mwai olandira thandizoli kuchokera ku bungwe la Higher Education Students Loans Board.
Izi zikutsatira kutsekulidwa kwa nthawi ya bungweli yolandira zikalata zofunsira thandizoli kuchokera kwa ophunzira ochepekedwawa.
Malingana ndi Dr Henry Chingaipe, yemwe ndi mmodzi mwa akulu akulu a bodiyi, nthawi yolembera kalata zofunsira chithandizochi yatsekulidwa lero pa 1 April, ndipo idzatsekedwa pa 30 mwezi wa mawa wa May.
Polankhula pa msonkhano wa olemba nkhani omwe anayitanitsa lero mu mzinda wa Blanyre, Chingaipe wati polemba kalatazo, ophunzirawa, mwa zina, asamayiwale kutumiza limodzi ndi chiphaso cha unzika, satifiketi ya Form 4 yowonetsa ma credit okwana asanu ndi imodzi (6), komanso chitupa cha pa sukulu yao.
Zonsenzi malingana ndi Chingaipe, zikuyenera kutumizidwa ku bungweli kudzera pa makina a pa Internet.
Ndalama zoposa K30 million ndi zomwe zayikidwa padera kuti zithandizire ophunzirawa chaka chino.