Chipani cha People’s Development PDP chasintha tsiku la zisankho zachipulula

Chipani cha People’s Development-PDP chalimbikitsa zokonzekera zake za ntchito yosankha odzachiyimira pa mipando ya aphungu a ku nyumba ya Malamulo pa chisankho chikudza cha patatu chomwe chichitike mdziko muno mu mwezi wa September.


Izi zikutsatira ganizo lake losintha tsiku lomwe ntchitoyi idzayambike mdziko muno.


Poyambilira, ntchitoyi yomwe idzachitike kudzera mu zisankho za chipulula, inakonzedwa kuti iyambike mu mwezi watha wa March.


Koma kamba ka kusinthaku, zisankhozi zikuyembekezeka kuchitika kuyambira pa 21 mwezi uno wa April.


Malingana ndi Rhodes Msonkho, yemwe ndi mneneri wa chipani cha PDP, masiku ochitira zisankho za chipulula anasinthidwa, mwa zina, powona kuchuluka kwa chiwerengero cha anthu ofuna kudzatenga nawo mbali pa zisankhozi.


Chomcho Msonkho wati chipanichi chinaona kuti kunali kwabwino kusintha tsikuli ndi cholinga chopereka mpata kwa anthu ambiri otenga nawo mbali pa zisankhozi.

Related posts

SULOM yapereka zifukwa zokwezera mtengo wa masewero

Boma lati lilemba ogwira ntchito za umoyo mdziko muno

Apolisi ati asintha kagwiridwe ka ntchito