Boma lati lilemba ogwira ntchito za umoyo mdziko muno

Boma lati lilemba ntchito ogwira ntchito za umoyo owonjezera mdziko muno.


Wafotokoza izi ndi nduna ya za umoyo Khumbize Kandondo Chiponda, pomwe dzulo amayankha mafunso kuchokera kwa aphungu aku nyumba ya malamulo.


Malingana ndi Chiponda, pa ntchitoyi, boma lilemba ogwira ntchito za umoyo okwana 6,700 kudzera mu ndondomeko ya chaka chino kufikira ya mawa, yomwe nyumbayi yavomereza sabata yatha.


Mwa ogwira ntchito za umoyowa ndi monga madotolo, anamwino ndi ma HAS.


Ndipo kuonjezera apo, ndunayi yati boma likhalanso likukweza pa ntchito omwe agwira ntchito za chipatala kwa nthawi yaitali mdziko muno.

Related posts

SULOM yapereka zifukwa zokwezera mtengo wa masewero

Apolisi ati asintha kagwiridwe ka ntchito

Olemba nkhani aziteteze pa nthawi yazipolowe