Mkulu wa a polisi mdziko muno Merlyn Yolamu walonjeza kuti awonetsetsa kuti a polisi akugwira ntchito zawo motsatira malamulo, pothana ndi mchitidwe wa ziwawa zokhudza ndale zomwe zamanga nthenje mdziko muno.
Lumbiroli laperekedwa dzulo pa mkumano omwe Yolamu anayitanitsidwa mu mzinda wa Lilongwe ndi komiti ya ku nyumba ya malamulo yowona za chitetezo.
Mkumanowu unayiyitanitsidwa, mwa zina, pofuna kumvetsetsa zomwe a polisi akuchita pofuna kuthana ndi mchitidwe wa zipolowe za ndale, pomwe pangotsala miyezi yowerengeka kuti zisankho zichitike mdziko muno.
Ndipo poyankhapo pa nkhaniyi, Yolamu mwa zina, analoza chala zipani za ndale zomwe anati chilichonse chili izo, zili ndi kagulu kochita za uchigawenga, komanso kulephera kwa apolisi wena kugwira ntchito yao pomwe za ntopola ngati izi zikuchitika.
Iye anati ndi zodabwitsa kuti a polisi wena akumalekelera za mtopola pomwe zikuchitika, zomwe anati zimasonyeza kulephera kwa a polisi ngati amenewa kugwira ntchito yao mwa ukadaulo.
Pamenepa iye walangiza a polisiwa kuti asamachite kudikilira chitsogozo cha iye kapena ma komishonala awo, pomwe pakufunika kudzetsa bata pomwe pabuka zipolowe za mtunduwu.
Chomcho iye wati nthambi ya apolisi ikhala ikuperekanso maphunziro kwa apolisiwa a momwe angathetsere ziwawa zokhudza ndale mdziko muno.