Zokonzekera zafika kumapeto mu mzinda wa Lilongwe za zionetsero zokwiya ndi kuchedwa kwa nyumba ya malamulo kukambirana nkhani yokhudza mulingo wa zaka zoyenereza oyimira pa mpando wa mtsogoleri wa dziko.
Omwe akuyembekezeka kuchita zionetserozi ndi achinyamata okhudzidwa mu mzinda wa Lilongwe.
Iwowa pakutha pa zionetserozi, zomwe zichitike kudzera mu ulendo wa ndawala, akapereka chikalata cha madandaulo awo pa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo.
Izi zikudza pomwe tikunena pano, malamulo amalora okhawo omwe afika zaka 35 kuyimira mpando wa mtsogoleri wa dziko.
Koma kuchoka pa zaka zaka 35, achinyamatawa omwe akutsogozedwa ndi Dennis Mahata – akufuna kuti zakazi zitsitsidwe kufika pa zaka zokwana 30.
Malingana ndi Mahata, zaka 35 zimapondereza ufulu wa achinyamatawa otenga nawo mbali pa chisankho cha mtsogoleri, komanso kutenga nawo gawo pa chitukuko cha dziko lino.

